Thursday, September 9, 2010

KHEMBO APEREKA UFA KU SANT’ EGIDIO

WOLEMBA WATIPASO MZUNGU JNR

   Ufa umene anapereka a Khembo
Nduna yoona anthu olumala ndi okalamba a Clement Khembo apereka matumba a ufa wa soya opyola 500 ku gulu la achinyamata losamalira anthu osauka ndi ana amasiye.

Polankhula atapereka mphatsoyo, a Khembo anati boma likuyamikira ntchito imene gulu la Community of Sant’ Egidio likugwira m’dziko muno makamaka posamalira anthu osauka, okalamba ndi ana amasiye.

“Ndizosangalatsa kuti pamene boma likuyesetsa kuchepetsa mavuto amene anthu okalamba ndi ana amasiye akukumana nawo, palinso achinyamata ngati inu amene mwadzipereka kuti muthandizepo,” anatero a Khembo.

“Ntchito yosamalira ana amasiye ndi okalamba si yaboma lokha, koma tonse. Inuyo ndi amene m’madziwa anthu ovutika chifukwa m’makhala nawo m’madera anu. Choncho ndibwino kuti udindo woyamba osamalira anthu ovutika ukhale m’manja mwanu, boma pambuyo,” anatsindika chomwechi andunawa.

M’modzi mwa ogwira ntchito ya chifundo mu gulu la Community of Sant’ Egidio a Francisco Zuze adati gulu lawo likukumana ndi mavuto ochuluka pantchito yawo kamba kosowa zipangizo zothandizira anthu osowa.

A Zuze anati ndizonyaditsa kuti boma kudzera mu unduna wa anthu olumala ndi okalamba laganiza kuti lithandize gululi ndi ufa womwe a Khembo anati uthandizire ana amasiye okhaokha.

“Matenda a Edzi apangitsa kuti ana amasiye achuluke tsiku ndi tsiku. Pamene chiwerengero cha anawa chikukwera gulu lathu limakhala likuchepa mphamvu zowathandizira anawa,” anadandaula a Zuze.

Yemwe amayang’anira ana amasiye ndi okalamba mu gululi mu chigawo cha pakati a Kondwani Hema anadandaulira ndunayo kuti anthu ena akumawanyogodola ponena kuti ndi amfiti eti kamba koti amagwirizana ndi nkhalamba.

“Kulikonse tingapite kuti tikapereke thandizo kwa okalamba, anthu otiwona amati ndife ophunzira ufiti n’chifukwa chake timagwirizana ndi azigogo otha mano mkamwa,” adatero a Hema.

A Khembo analonjeza achinyamatawo kuti boma likhazikitsa mfundo zoti munthu aliyense onena anthu okalamba kuti ndi mfiti adzitengedwera ku bwalo lamilandu kuti adzikamangidwa ndi kukagwira ndende.

Yatha

No comments: