Wednesday, October 13, 2010

Mfundo za WHO pa fodya zikwiyitsa Africa

Wolemba:Watipaso Mzungu Jnr

Nthumwi zochokera mayiko 11 omwe amalima fodya ati ndi okwiya ndi mfundo zomwe bungwe la  za umoyo pa dziko lapansi, World Health Organization (WHO), likufuna kukhazikitsa pa ulimi wa fodya ndipo zagwirizana kukatsutsa malamulowo pa msonkhano womwe udzachitikire ku Uruguay mwezi wa November chaka chino.
Bungwe la WHO likufuna kuthetsa ulimi wa fodya wa bale ndi oriental, iwo akuti fodyayu ali ndi zinthu zina zimene zitha kuyambitsa matenda kwa osuta.
Koma pamsonkhano umene udachitikira ku Lusaka dziko la Zambia sabata latha, nthumwi zochokera ku Zimbabwe, Tanzania, Mozambique, Malawi, Uganda, Madagascar, Swaziland, Cote d’Ivoire, Ethiopia komanso Zambia zidagwirizana kukatsutsa mfundozi ati chifukwa choti mfundozo zitha kubweretsa umphawi kwa anthu a mu Africa.
M’chikalata chimene adatulutsa pakutha pa msonkhanowo, nthumwizo zidati kuthetsa ulimi wa fodya kutha kubweretsa mavuto owopsa monga njala ndi kusowa kwa ndalama.
“Fodya ndi mbewu yokhayo yodalirika imene imatibweretsera ndalama zakunja m’mayiko mwathu. Anthu ambirimbiri atha kuvutika kwambiri WHO itathetsa malonda komanso ulimi wa fodya,” chidatero chikalatacho.
Ndipo mkulu wa bungwe la alimi a fodya ku Zambia, Tobacco Association of Zambia, a Knox Mbazima adati anthu ochuluka amene amadalira ulimi wa fodya mu Africa adzasowa mtengo wogwira.
“Ngati mfundozi zingavomerezedwa ndi kugwiritsidwa ntchito, anthu ambiri adzachotsedwa ntchito m’makampani omwe amagula ndi kugulitsa fodya, mayiko a mu Africa adzasowa ndalama zakunja komanso mfundozi zidzabweretsa umphawi kaamba koti palibe mbewu ina panopa imene ingalowe mmalo mwa fodya,” adatero a Mbazima.
Dziko la Malawi lati ilo ndilokonzeka kumenyera ufulu wa alimi a fodya. Wachiwiri kwa nduna ya za malonda ndi mafakitale, a Shadreck Jonasi, adati iwo alembera kale ma bungwe a COMESA ndi SADC pakusagwirizana kwawo ndi malamulo atsopano a WHO.
“Amalawi oposa 750,000 adzavutika kowopsa ngati malamulowa angadzavomerezedwe. Komanso chuma cha dziko lino chidzakhudzidwa kwambiri poti ife timadalira ulimi wa fodya pa ndalama za kunja kwa dziko lino,” a Jonasi adatero.
Malawi ndi limodzi mwa mayiko a mu Africa amene amalima fodya wapamwamba ndi kumugulitsa yense ku makampani akunja omwe amapanga ndudu komanso zinthu zina kuchokera ku fodya.
[Yatha]

No comments: