Wednesday, October 13, 2010

Mutharika alephera kukhala nawo pa mapemphero a zaufulu

Wolemba: Watipaso Mzungu Jnr

Msonkhano wa mapemphero opempherera mavuto apa dziko lonse la pansi umene udachitikira ku Barcelona masiku apitawa, Pulezidenti Bingu wa Mutharika adalephera kukakhala nawo kaamba koti adatanginidwa ndi ntchito zina ku US, Iran ndi Germany.
Mapempherowo adakonzedwa ndi bungwe la Community of Sant’ Egidio ndi mutu woti: “Kukhala limodzi nthawi ya mazunzo. Banja la anthu a mafuko osiyanasiyana, banja la Mulungu”.
Mlangizi wa Pulezidenti pa nkhani za chipembedzo, Mbusa Billy Gama, adatsimikiza za nkhaniyi. Koma iwo adati Mutharika sadakatha kukhala nawo pa mampherowo kaamba koti adatanganidwa ndi ntchito zina.
Mmodzi wa akuluakulu a bungwe la Sant’ Egidio, a Franciso Zuze adati Mutharika adayitanidwa ngati wapampando wa bungwe la African Union (AU) ndipo amayenera kulankhula moyambilira.
A Zuze adati Mutharika ali ndi udindo wawukulu pa ntchito yothetsa mavuto omwe dziko la Africa likukumana nawo monga njala, umphawi, mavuto a zachuma komanso mikangano pa ndale m’mayiko a mu Africa.
“Africa ikukumana ndi mavuto ambiri a zachuma, kusagwirizana pakati pa zipani zolamula ndi zotsutsa komanso umphawi. Choncho nkofunikira kuti adayenera kukhala nawo,” adatero mkuluyu.
Gama adati ngakhale Mutharika adalonjeza kukakhala nawo pa msonkhanowo, koma sadakatha kaamba koti msonkhanowo udachitika pa nthawi imene ankagwira ntchito zina ku US, Iran ndi Cuba.
M’malo mwake, Mutharika adatuma nduna ya za ulimi a Peter Mwanza, Nicholas Dausi, ma bishopu opuma awiri; Allan Chamgwera ndi Felix Mkhori komanso Gama kuti akawayimire.
Koma, a Mkhori sadathe kupita nawo malinga ndi zifukwa zina.
Enanso omwe adayitanidwa ku msonkhanowo ndi a zipembedzo cha Chisilamu, Chiyuda komanso azipembedzo Chamakolo.
[Yatha]

No comments: